Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:65 - Buku Lopatulika

65 Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

65 Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

65 Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri a ku Yudeya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

65 Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:65
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda;


Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.


Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.


Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.


Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.


Ndipo anadza mantha aakulu pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumva izi.


Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.


Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.


Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.


Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa