Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:19 - Buku Lopatulika

19 Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Maiyo adati, “Bambo, ndadziŵa tsopano kuti ndinu mneneri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:19
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeze kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo ino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi?


Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;


Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.


pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu.


Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.


Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa