Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:18 - Buku Lopatulika

18 pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:18
16 Mawu Ofanana  

Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.


Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?


Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova.


Ndiwe mkazi wokwatibwa wochita chigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wake.


Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:


Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;


ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.


Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.


Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe;


Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.


Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa