Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:20 - Buku Lopatulika

20 Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:20
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.


Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.


Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.


Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.


pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,


koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.


Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?


Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene munkako kulilandira, munene mdalitso paphiri la Gerizimu, ndi temberero paphiri la Ebala.


Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa