Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:14 - Buku Lopatulika

14 Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:14
18 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;


Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.


Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.


Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.


ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.


Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?


Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu.


Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa