Luka 19:44 - Buku Lopatulika44 ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang'aniridwe ako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201444 ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang'aniridwe ako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa44 Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero44 Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.” Onani mutuwo |
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.