Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:8 - Buku Lopatulika

8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, “Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!”

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:8
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?


Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?


Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani? Ndigwira pakamwa.


Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.


Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.


Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukulu.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.


ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.


Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;


Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.


Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,


Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.


Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa