Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;
Eksodo 7:14 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Farao ndi wokanika kwambiri, akukana kulola anthu anga kuti apite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;
Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.
Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'mtsinje mokha.
Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake.
Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.
koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.
Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?