Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 12:25 - Buku Lopatulika

25 Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba?

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:25
36 Mawu Ofanana  

Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.


Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira;


Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba.


Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa; koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.


Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.


Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.


Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi ino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.


Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.


Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.


Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m'chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.


Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.


Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.


Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukacheteka, ndi kugwadira milungu ina ndi kuitumikira;


Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo padziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.


ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?


Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;


Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.


Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa