Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 7:12 - Buku Lopatulika

12 Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 7:12
34 Mawu Ofanana  

Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.


koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.


Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?


Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mau anga.


Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.


Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutali ndi chilungamo;


Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwere nacho.


Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.


koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo.


Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.


Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;


kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.


Ndipo anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu.


Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.


Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.


Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?


Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.


kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.


Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.


pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse.


pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa