Zekariya 7:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Poti sadandimvere nditaŵaitana, Inenso sindidaŵamvere atandiitana. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 “ ‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.