Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 7:14 - Buku Lopatulika

14 koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Monga momwe amachitira kamvulumvulu, ndidaŵamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu imene iwo sankaidziŵa, ndipo dziko lao lidasanduka chipululu, kotero kuti palibenso wina amene ankayendamo. Choncho dziko lao lokomalo lidasandukadi chipululu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 ‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 7:14
35 Mawu Ofanana  

kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.


Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.


Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.


Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa.


Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.


Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.


Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, chatuluka, chimphepo chakukokolola: chidzagwa pamutu pa oipa.


Ndipo akulu anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.


Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.


Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.


chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.


nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala mu Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo.


Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikuchokere.


Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.


Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum'mawa, ndi kudziko lokometsetsa.


Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvere Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.


Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.


Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;


Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.


Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.


Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,


Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.


Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa