Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 38:9 - Buku Lopatulika

Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zochingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adapanga bwalo. Nsalu zake zochingira bwalolo chakumwera kwake zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo kutalika kwake kunali mamita 46.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.

Onani mutuwo



Eksodo 38:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.


Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.


Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.


Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.


Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.


nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva.


Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.


Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo.


ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.


ndi nsalu zotchingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa chihema ndi paguwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.