Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 38:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zochingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono adapanga bwalo. Nsalu zake zochingira bwalolo chakumwera kwake zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo kutalika kwake kunali mamita 46.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anamanga bwalo la mʼkati lokhala ndi khoma lokhala ndi mizere itatu ya miyala yosema ndiponso mzere umodzi wa matabwa osemedwa a mkungudza.


Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.


Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.


Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo.


Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.


odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.


“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.


Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.


Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.


Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.


ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo.


makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa