Eksodo 38:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Ndipo adapanga beseni lamkuŵa losambira, pamodzi ndi phaka lake. Adapanga zimenezi ndi akalilole a akazi amene ankatumikira ku chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano chija, kumene Chauta ankakumanako ndi anthu ake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano. Onani mutuwo |