Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 38:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono guwalo pomalinyamula, mphikozo ankazilonga m'mphete zija, pa mbali zonse ziŵiri za guwa. Guwalo adalipanga ndi matabwa, ndipo adalijoba m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:7
5 Mawu Ofanana  

Napanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi mkuwa.


Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.


Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;


koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.


Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa