Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 4:26 - Buku Lopatulika

26 ndi nsalu zotchingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa chihema ndi paguwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 ndi nsalu zochingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa Kachisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:26
4 Mawu Ofanana  

Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;


zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao;


Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;


Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa