Eksodo 26:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo uzipanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 “Upange chihema chamapemphero ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Nsalu zimenezi uzipete bwino ndi zithunzi za akerubi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi. Onani mutuwo |