Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 26:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo uzipanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Upange chihema chamapemphero ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Nsalu zimenezi uzipete bwino ndi zithunzi za akerubi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:1
29 Mawu Ofanana  

mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”


Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa.


Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”


Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni.


Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho,


Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi;


“Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo.


Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri.


“Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi.


“Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.


Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti,


Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake;


Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko.


nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi;


Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi.


Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso.


“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.


Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano,


Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano,


Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.


Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.


Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.


Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.


Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo.


Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada kuti avale.” (Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).


Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa