ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ahebri 1:1 - Buku Lopatulika Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;
Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inu mdulidwe (si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.
Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;
Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.
amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,
tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;
Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;
Koteronso Khristu sanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe.
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,