Ahebri 3:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Mose anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu ngati wantchito chabe, kuti achitire umboni zimene Mulungu analikudzanena m'tsogolo mwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. Onani mutuwo |
Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji paphiri la Gerizimu, ndi ena pandunji paphiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.