Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:55 - Buku Lopatulika

55 (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse monga ananena kwa makolo athu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:55
12 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.


Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.


Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.


m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.


ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;


mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.


Anathangatira Israele mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo,


Ndipo Maria anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa