Yohane 16:13 - Buku Lopatulika13 Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. Onani mutuwo |