Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 3:21 - Buku Lopatulika

21 amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Iyeyo anayenera kukhala Kumwamba mpaka nthaŵi yakukonza zonse kwatsopano, monga Mulungu adanenera kuyambira kalekale mwa aneneri ake oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 3:21
16 Mawu Ofanana  

ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.


Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,


amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu;


kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


kuti mukumbukire mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu;


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa