Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 5:5 - Buku Lopatulika

5 Koteronso Khristu sanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koteronso Khristu sanadzilemekeza yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 5:5
12 Mawu Ofanana  

Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.


Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;


kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe? Ndiponso, Ine ndidzakhala kwa Iye Atate, ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?


Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.


Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;


wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa