Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 9:19 - Buku Lopatulika

19 Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Poyamba Mose adaalengeza kwa Aisraele malamulo onse, motsata Malamulo amene Mulungu adaampatsa. Pambuyo pake adatenga magazi a anaang'ombe amphongo ndi madzi, nawaza pa buku la Malamulo ndi pa anthu onse. Adaachita zimenezi ndi kanthambi ka chitsamba cha hisope, ndiponso ndi ubweya wankhosa wofiira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:19
26 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.


momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.


Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;


ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.


Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yaikazi.


Ndipo anavula malaya ake, namveka malaya ofiira achifumu.


Ndipo anamveka Iye chibakuwa, naluka korona waminga, namveka pa Iye;


Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.


Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa;


Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.


Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;


momwemo choyambachonso sichinakonzeke chopanda mwazi.


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa