Afilipi 2:22 - Buku Lopatulika Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake. |
Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;
Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.
Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.
Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu.
Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.
Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.
Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;
chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.