Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:24 - Buku Lopatulika

24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono muŵatsimikizire chikondi chanu, kuti mipingo yonse ichiwone, ndi kudziŵa kuti sitikulakwa tikamakunyadirani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:24
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.


Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.


Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa