Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 1:7 - Buku Lopatulika

7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndikuyeneradi kuganiza zotere za nonsenu, popeza kuti ndimakukondani kwambiri. Pakuti nonsenu ndinu ogwirizana nane ndithu, pamene ndili m'ndende ndiponso pamene ndikugwira ntchito iyi imene Mulungu adandipatsa mwa kukoma mtima kwake, ntchito ya kuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 1:7
34 Mawu Ofanana  

koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.


Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?


chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.


Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.


Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;


Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.


Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,


chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.


Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;


kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m'bwalo lonse la alonda, ndi kwa ena onse;


ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;


Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.


Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.


Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.


Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu.


ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,


pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;


Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;


m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.


Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino:


Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;


koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.


Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:


Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;


Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa