Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 3:39 - Buku Lopatulika

Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!”

Onani mutuwo



2 Samueli 3:39
30 Mawu Ofanana  

Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?


Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.


Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?


Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?


Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.


Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.


Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakhwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire.


Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.


Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwapambana.


Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.


Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo.


Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.


Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.


Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.


Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.


Mfumu yokhala pa mpando woweruzira ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.


Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.


Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.


nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.


Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu.


Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.


Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.


pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.


Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;


Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.