2 Samueli 19:22 - Buku Lopatulika22 Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Koma Davide adayankha kuti, “Za ine zikukukhudzani bwanji, inu ana a Zeruya, kuti lero lino mukhale ngati adani anga. Kodi lero m'dziko la Israele nkuphamo munthu? Kodi sindikudziŵa kuti tsopano ndine mfumu ya Aisraele?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?” Onani mutuwo |