2 Mbiri 13:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwapambana. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Ndipo anthu ena achabechabe adasonkhana kwa iye nachita chipongwe Rehobowamu mwana wa Solomoni pa nthaŵi imene Rehonowamu anali wamng'ono ndi wosalimba mtima, ndipo sankatha kulimbana nawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Ndipo anthu ena achabechabe anasonkhana kwa iye ndipo anatsutsana ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni pamene anali wamngʼono ndi wosalimba mtima ndi wopanda mphamvu kuti athe kulimbana nawo. Onani mutuwo |
Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.