Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 6:16 - Buku Lopatulika

16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Choncho mfumu inalamula, ndipo anabwera naye Danieli ndi kukamuponya mʼdzenje la mikango. Mfumu inati kwa Danieli, “Mulungu wako amene umutumikira nthawi zonse, akupulumutse!”

Onani mutuwo Koperani




Danieli 6:16
28 Mawu Ofanana  

Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Koma ine, taonani, ndili m'manja anu; mundichitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.


Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.


Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?


Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?


Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.


Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.


Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.


Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?


Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo:


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa