Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ndipo mukauze Amasa mau anga oti, ‘Kodi iwe, sindiwe mbale wanga weniweni?’ Ndithu Mulungu andilange, mpaka ndife ndithu, ngati sindikuika iwe kuti ukhale mkulu wankhondo m'malo mwa Yowabu kuyambira tsopano lino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:13
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati kwa iye, Eetu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.


Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.


Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.


Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.


Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,


Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.


kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa