Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.
2 Samueli 24:14 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adauza Gadi kuti, “Iyai, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde, tisagwe m'manja mwa anthu ai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.” |
Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.
Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mzinda ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?
Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.
Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;
Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.