Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 1:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndaŵakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene ali pa mtendere. Pamene ndinkakwiyira anthu anga motsinira, mpamene anthu enawo ankakakatira kuzunza anthu anga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.’

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:15
28 Mawu Ofanana  

Aipsa njira yanga, athandizana ndi tsoka langa; ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.


Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza.


Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.


Pakuti alondola amene Inu munampanda; ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.


M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.


Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.


Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.


Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala mu Kasidi zoipa zao zonse anazichita mu Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.


Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;


Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!


Munaponda dziko ndi kulunda, munapuntha amitundu ndi mkwiyo.


Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.


Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.


Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao.


Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko la kumpoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa