2 Samueli 24:13 - Buku Lopatulika13 Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Choncho Gadi adadza kwa Davide, namuuza kuti, “Musankhe, kodi pabwere zaka zitatu zanjala m'dziko mwanu, kapena inu mukhale mukuthaŵa adani anu pa miyezi itatu, kapena pakhale mliri wa masiku atatu m'dziko mwanu? Ganizani bwino, ndipo mutsimikize chilichonse choti muyankhe, kuti ine ndikauze amene adanditumayo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.” Onani mutuwo |
kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?