Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 24:12 - Buku Lopatulika

12 Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Pita ukamuuze Davide kuti, ‘Ine Chauta ndikunena kuti, “Ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchite. Tsono usankhepo chimodzi, ndipo ndidzakuchita.” ’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:12
13 Mawu Ofanana  

Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.


Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,


Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.


Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwe m'buku la mbiri ya mfumu Davide.


pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.


Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.


Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;


Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa