Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yona 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka.

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:2
24 Mawu Ofanana  

Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.


Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.


Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake.


ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chao, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire.


Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.


Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.


Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.


Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.


Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa