Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 24:15 - Buku Lopatulika

15 Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikira; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Choncho Chauta adagwetsa mliri pa Aisraele, kuyambira m'maŵa mpaka pa nthaŵi imene adaafuna mwini wake, mwakuti kuchokera ku Dani mpaka ku Beereseba adafa anthu okwanira 70,000 pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:15
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu.


Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele.


Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwe m'buku la mbiri ya mfumu Davide.


Woyang'anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.


Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.


Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.


Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.


Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa