Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:6 - Buku Lopatulika

6 Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pamene Aisraele adaona kuti ali m'zoopsa, poti anali atapanikizidwadi kwambiri, adakabisala m'mapanga, m'maenje, m'matanthwe, m'makwaŵa ndi m'zitsime.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:6
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.


Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.


Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.


Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.


Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;


(amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.


Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mzinda unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa.


Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele.


Natembenuka amuna a Israele; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti chidawagwera choipa.


Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.


Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.


Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala.


Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko.


Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?


Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo.


Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.


Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa