Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Afilisti adasonkhana pamodzi kuti amenyane nkhondo ndi Aisraele. Adasonkhanitsa magaleta ankhondo 30,000, okwera pa akavalo 6,000 ndi ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Iwowo adapita nakamanga zithando zao ku Mikimasi, kuvuma kwa Betaveni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:5
21 Mawu Ofanana  

kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.


Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.


Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.


Wafika ku Ayati, wapitirira kunka ku Migironi; pa Mikimasi asunga akatundu ake;


mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.


Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Ombani mphalasa mu Gibea, ndi lipenga mu Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.


Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.


Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.


Ndipo malire ao a kumpoto anachokera ku Yordani; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi matulukiro ake anali ku chipululu cha Betaveni.


Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.


Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.


Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafike masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;


Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.


Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.


Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.


Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.


Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa