Lamulira iwo achuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,
Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo.
Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,
Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.
Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.
Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.
Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;
ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Ndili nacho chiyembekezo popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,
chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.
Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.
Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.
Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.
Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu.
Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.
Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu.
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.
Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;
popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.
Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?
Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.
Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.
Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.
Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?
Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.
chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;
Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.
Chilungamo chanu sindinachibisa m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisira msonkhano waukulu.
Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova.
Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.
Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede.
Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.
Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.
Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.
Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.
Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa la kuthengo.
Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.
Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.
Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:
Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.
Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.
Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;
amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:
Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.