Ndikufuna ndikuuzeni za mphatso yochokera kwa Mulungu, mphatso ya ubatizo wa Mzimu Woyera. Mphatso imeneyi ndi ya aliyense amene amakhulupirira Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wawo. Ndi chinthu chosangalatsa chomwe chimasintha moyo wanu ndi kukupatsani mphamvu ya Mulungu.
Ubatizo wa Mzimu Woyera ndi chochitika chapadera chomwe simungaiwale. Baibulo limanena kuti ndi kudzazidwa ndi Mzimu (Aefeso 5:18) ndi kulandira mphamvu kuti mukhale mboni za Yesu (Machitidwe 1:8). Zimakuthandizani kukhala moyo woyera, kubala zipatso zabwino, ndiponso kugwiritsa ntchito mphatso zauzimu potumikira Mulungu ndi mpingo wake.
Ubatizo wa Mzimu Woyera ndi wofunika kwambiri kwa okhulupirira. Ndi ntchito ya Mzimu Woyera yomwe imalimbitsa ubale wanu ndi Mulungu, imakupatsani mphamvu kuti mupambane pa moyo wanu, ndiponso imakukonzeretsani kutumikira mu Ufumu wake.
Sindikudziwa ngati mwakhala mubatizidwa ndi Mzimu Woyera, koma ngati simunalandire mphatso yokongola iyi, ndikukupemphani kuti mupemphere. Mupemphe Mzimu Woyera kuti akutsanulireni moto wake ndi kukhala nanu. Muzipempha ndi mtima wonse, osaleka mpaka mutaona mphamvu yake m'moyo wanu. Musachite mantha, ndikukutsimikizirani kuti mudzakhala ndi chimwemwe chachikulu chomwe sichidzachoka m'mutu mwanu.
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.
pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;
Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.
ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.
Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,
Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja. Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.
ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa. Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika. Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma. Pamene anatuma ku Masedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi m'Asiya. Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo. Pakuti munthu wina dzina lake Demetrio wosula siliva, amene anapanga tiakachisi tasiliva, ta Aritemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri; amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza chuma chathu. Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja: ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza. Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, nafuula, nati, Wamkulu ndi Aritemi wa ku Efeso. Ndipo m'mudzi monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo. Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane. Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, ophunzira ake sanamloleza. Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ake, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye kubwalo lakusewera. Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa chifukwa chake cha kusonkhana. Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo. Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akufuula monga maora awiri, Wamkulu ndi Aritemi wa Aefeso. Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi? Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu kaliuma. Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano. Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane. Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa. Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu. Pakutinso palipo potiopsa kuti adzatineneza za chipolowe chalero; popeza palibe chifukwa cha kufotokozera za chipiringu chimene. Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano. Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.
Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.
Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.
Ndipo sindinamdziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.
Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake. Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.
Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife; ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.
Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.
Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu.
Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?
Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.
Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye; Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kachisi; ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu;
Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;
kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.
Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu. Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.
Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova.
Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.
m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.
Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. m'Frijiya, ndiponso m'Pamfiliya, m'Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu. Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani? Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero. Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga. Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku; komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele, Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda. Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa. Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!
Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.
a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.
Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.
Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.
Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?
Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena; Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki. Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo; kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka. Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene anachita ichi. Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani? Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa. Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika. Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao. Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu. ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.
iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.
Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa la kuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma: Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m'mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa. ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime. Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.
Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukana nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.
Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse. ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,
Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;