Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


70 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Mzimu Woyera

70 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Mzimu Woyera

Mukadzapeza mphamvu ya Mzimu Woyera, mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya konse, ku Samariya, ndi kufikira malekezero a dziko lapansi. (Machitidwe 1:8) Mzimu Woyera ndi wofunika kwambiri pa moyo wanga ngati chakudya chimene ndimadya tsiku ndi tsiku, ndi ngati madzi amene amachirikiza thupi langa. Mphamvu imeneyi ndi yofunika kwambiri kuti ndigone nkhondo ndi mayesero amene ndimakumana nawo.

Mphamvu ya Mzimu Woyera ikagwira ntchito mwa ine, imandipanga kukhala munthu watsopano. N’chifukwa chake ndimapemphera kuti Mzimu Woyera akhale ndi ine nthawi zonse. Amandipatsa mphamvu panthawi ya mavuto, amandipatsa chigonjetso pa mayesero, ndipo amandilimbitsa m’dziko lino lodzaza ndi zinthu zosokoneza.

Mzimu Woyera ndi mphatso yabwino kwambiri imene ndili nayo. Ulemerero wake umasandutsa ukapolo kukhala ufulu, umasandutsa mkuntho kukhala mtendere, ndipo umasandutsa kusowa chiyembekezo kukhala chikhulupiriro. Sindingasiye kuyenda ndi Mzimu wa Mulungu; ndiyenera kumulola kuti anditsogolere ndi kundipatsa madzi a moyo wake kuti ndikhale moyeretsa ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha umene Mulungu anakonzeratu onse amene amamukonda.




Aroma 15:19

mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:11

Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:35

Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:4

Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:14

Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 3:8

Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:7-8

Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu? Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:5

kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:49

Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 3:17

Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 4:6

Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:27

Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:16

Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:5

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:5

Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:10

Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:14

Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:11

Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4

Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:32

Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13

Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:21

pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:7

Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:4-5

ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:4-5

Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:26

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:18

Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:31

Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:16

Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:13

Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:17

Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:6

Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26-27

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:3

Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:17-18

Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:30

Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:2

Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9

Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:2

monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:27

kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:4

pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:6

Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:28

Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44-45

Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:52

Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:19

Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:33

Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:20

Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:33

Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:13-14

Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:14

Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:6-7

Ndipo anapita pa dziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo. Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu. Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wokondedwa, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu! Yesu, zikomo chifukwa cha Mzimu Woyera wanu, ndikupemphani kuti mphamvu yanu itsanulidwe pa mpingo wanu, kuti mutiyimikitse mu ulamuliro wanu, kuti tisagonjetsedwe ndi kukhazikika m'mawu anu, kuti kulikonse kumene tipita mphamvu yanu iwonekere ndipo miyoyo isinthe, khalani inu mukuyatsa moto m'miyoyo yathu, kumene tikuona zodabwitsa zanu, zizindikiro ndi zozizwitsa. Mawu anu alalikidwe ndi mafuta ndi moto wa Mzimu Woyera wanu. Inu mwanena m'mawu anu: "Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzakugwerani; ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya yonse, ndi ku Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko lapansi." Ambuye Yesu, mphatso za Mzimu Woyera wanu ziwonekere pa Mpingo ndipo ziononge ndi moto wanu chilichonse chomwe si chanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa