Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

208 Mau a m'Baibulo Okhudza Ufiti ndi Zamatsenga


Deuteronomo 12:3

nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:36

Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha:

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 46:5-7

Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?

Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.

Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 4:8

Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:16

Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza;

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:13

Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:22-23

Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 34:14

pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:20-21

Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:4-7

Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu.

Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya;

makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;

manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 11:14-15

Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.

Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Danieli 3:18

Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:3-5

Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.

Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko.

Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 4:23-24

Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 97:7

Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 42:8

Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 135:15-18

Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu.

Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya;

makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya.

Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:8

Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 51:17-18

Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m'menemo.

Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 45:20

Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 10:3-5

Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa.

Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.

Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 2:18

Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:26

Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 10:13-14

Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,

osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 21:6

Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 5:12

ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:18

Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 18:10-12

Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.

Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.

Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 47:12-14

Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.

Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 20:27

Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 20:6

Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 33:6

Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,

Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.

kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,

njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 21:8

Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 22:15

Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 27:9

Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babiloni;

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 16:16-18

Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.

Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.

Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:31

Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 41:8

Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 28:7-9

Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.

Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake.

Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:43-45

Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.

Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.

Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 4:12

Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 19:18-19

Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao.

Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 23:23

Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 44:25

Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 18:23

ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 9:20-21

Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

ndipo sanalapa mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:6

Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 10:2

Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 14:14

Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 17:17

Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 22:28

Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 21:21

Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 13:6-9

Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.

Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanena?

Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.

Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:23

Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 28:7

Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 4:19

ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 23:24

Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 44:6

Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 96:5

Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 32:17

Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 10:13

Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 5:26

Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 3:2-3

munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza ndi mneneri, ndi waula, ndi nkhalamba;

ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri;

mphete, ndi zipini;

malaya a paphwando, ndi zofunda, ndi zimbwi, ndi timatumba;

akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba.

Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.

Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m'nkhondo.

Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.

kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi mphungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:28

Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori, nadyanso nsembe za akufa.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 4:6

Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 17:2-5

Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake,

kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, m'ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.

nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;

ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsira, ndipo taonani, chikakhala choonadi, choti nzenizeni, chonyansachi chachitika m'Israele;

pamenepo mutulutse mwamunayo kapena mkaziyo, anachita choipacho, kunka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 28:3

M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika m'Rama, m'mudzi mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 29:8

Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 8:19-20

Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?

Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.

Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 47:9

koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 7:11-12

Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.

Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 18:14

Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 19:19

Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:22

Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 23:5

Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 13:1-5

Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa;

Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo.

Kuti Israele wonse amve, ndi kuopa, ndi kusaonjeza kuchita choipa chotere chonga ichi pakati pa inu.

Ukamva za umodzi wa midzi yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,

Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mudzi mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwa;

pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, chikakhala choona, chatsimikizika chinthuchi, kuti chonyansa chotere chachitika pakati pa inu;

muzikanthatu okhala m'mudzi muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuononga konse, ndi zonse zili m'mwemo, ng'ombe zake zomwe, ndi lupanga lakuthwa.

Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.

Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;

pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino, kuchita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziwa, ndi kuitumikira;

musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.

Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:37-38

Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,

nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:16

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 13:20

Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 7:25-26

Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.

Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:13

Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 14:6

Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:14

Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:21

Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:5

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:7-8

ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:31

Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:21-23

chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.

Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:1

Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:1

Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 101:3

Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;

umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:15

Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:8

Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 16:17-18

Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.

Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:8-9

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:7

Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:14

Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 14:9

Ndipo akacheteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamcheta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:27

Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:20

kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:22

Mupewe maonekedwe onse a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 13:6-8

Ndipo m'mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu;

ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 47:1-3

Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.

Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.

Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.

Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.

Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.

Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.

Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.

Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 81:12-13

Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.

Ha! Akadandimvera anthu anga, akadayenda m'njira zanga Israele!

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 29:18

kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:8

Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 4:10

Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:16-17

Musanyengedwe, abale anga okondedwa.

Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 3:1

Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pa maso panu, wopachikidwa?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:24-27

Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.

Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;

ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?

Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 10:19

Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:14-16

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:21

Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:11-12

Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:14-17

Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?

Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:19

Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:7

Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?

Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:7-8

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:13

Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:3-5

Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.

Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:1-5

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.

Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.

Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.

Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa la kuthengo.

Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.

Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.

Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.

Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.

Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;

amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:

Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:19-20

Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;

nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse;

kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:11

Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 2:10-15

Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,

kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza;

kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota;

akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima;

omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa;

amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,

ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.

Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1-3

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.

Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:4-5

Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.

Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:33

Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:1-3

Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.

Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.

Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka.

Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.

Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu, mundipulumutse ndi chifundo chanu.

Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.

Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.

Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!

Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.

Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

Wolemekezeka Yehova, pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa m'mudzi walinga.

Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.

Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:17-19

Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse.

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1-3

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.

Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:17

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3-5

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:5-6

Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.

Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:23

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 1:10-11

Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;

pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:1-2

Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve;

Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa.

Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.

Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;

ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.

Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.

Inde choona chisoweka; iye amene asiya choipa, zifunkhidwa zake; ndipo Yehova anaona ichi, ndipo chidamuipira kuti palibe chiweruzo.

Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza.

Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda.

Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango.

Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.

koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.

Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 51:6-7

Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:15

Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:22

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 10:13

pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:1-5

Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,

Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;

kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.

Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.

Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,

atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;

ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;

ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;

kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.

Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;

zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;

omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;

mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye;

chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;

koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,

tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:37

Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,

Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.

Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;

ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe.

Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;

kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya.

Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeza malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.

Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;

Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:24

chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:24

Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:2

Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:12

Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:30

Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:11-12

ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:20

Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 95:7-8

Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!

Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 5:30-31

Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m'dzikomo;

aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 99:8-9

Munawayankha, Yehova Mulungu wathu: munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira, mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.

Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani pa phiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:1

Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 13:18

nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 18:20-21

Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israele, namemeza aneneri onse kuphiri la Karimele.

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:20-22

Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israele, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israele, ntheradi.

Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.

Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:10

amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:18-20

Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu.

Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi.

Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 27:15

Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 4:24

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 32:16-17

Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo, anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa.

Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 34:13-14

koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 7:2

nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:36-39

Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha:

Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,

nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:3-4

anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;

amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:23-25

Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musamvomereze;

chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:18-23

Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;

chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo.

umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m'malembo oyera,

Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.

Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:6-9

Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;

umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.

Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.

Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:1-3

Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.

koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;

popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano.

Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,

ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m'madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;

okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;

posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;

koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.

Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.

Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo;

ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali akapolo a chivundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake.

Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.

Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.

Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

Chidawayenera iwo cha nthanthi yoona, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.

Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwa ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.

Mutu    |  Mabaibulo