Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


109 Mau a m'Baibulo Okhudza Miseche

109 Mau a m'Baibulo Okhudza Miseche

M'mavesi osiyanasiyana a m'Baibulo, tikulimbikitsidwa kuti tisamachite miseche. Mwachitsanzo, mu bukhu la Aefeso 4:29, limatiuza kuti, "Mawu alionse oipa asatuluke m'kamwa mwanu, koma oti angakhoze kulimbikitsa ena, malinga ndi chifuniro chawo, kuti apereke chisomo kwa iwo akumva."

Mulungu akufuna kuti mawu athu akhale olimbikitsa ndi omanga, osati owononga. Tikamanena miseche, sitikungowononga mbiri ya munthu wina, koma tikuwononganso yathu, chifukwa mawu athu amasonyeza umunthu wathu ndi makhalidwe athu.

Baibulo limatilangizanso kufunika kwa chilungamo ndi choonadi. Mu Levitiko 19:16 limati, "Usamanene miseche pakati pa anthu a mtundu wako; usaime moyo wa mnansi wako: Ine ndine Yehova."

Ndikufuna kukuuzani kuti Baibulo limatiuza kuti tisamale ndi mawu athu ndikupewa miseche. M'malo moipitsa ndi kuwononga mbiri ya ena, tiyenera kukhala anthu olankhula zoona, chilungamo, ndi mawu olimbikitsa.

Motsatira mfundo izi za m'Baibulo, tidzathandiza kumanga dziko lomwe miseche siilipo, komanso lomwe ulemu ndi choonadi zimalamulira. Zikomo.




Yakobo 4:11

Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:16

Usamnamizire mnzako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:10

Usanamizire kapolo kwa mbuyake, kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:18

Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:5

Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:16

ndi kukhala nacho chikumbu mtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Khristu akachitidwe manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:5

Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:9

Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:10

Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:20

Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:21-23

Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:22

Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:8

Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:3

Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31

Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:1-3

Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:16

Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:28

Munthu wokhota amautsa makani; kazitape afetsa ubwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:12

ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-30

anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 120:1-2

Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza. Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:13

Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mau.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 9:4-6

Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi. Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa. Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:13

ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:13

Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:2

asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:1

Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:5

Mboni yokhulupirika sidzanama; koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:11

Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:18

Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:19-20

Pakamwa pako mpochita zochimwa, ndipo lilime lako likonza chinyengo. Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro. Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:18

Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:4

Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:6

sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 120:2-3

Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga. Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:8

Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka, zotsikira m'kati mwa mimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:45

Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:6

Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:2-4

Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo, ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:9

Woyenda moongoka amayenda osatekeseka; koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:20

Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:28

Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa; kodi udzanyenga ndi milomo yako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:4

Wochimwa amasamalira milomo yolakwa; wonama amvera lilime losakaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:3

Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:17-18

Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:13

Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 39:1

Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:19

Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:2-3

pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza. Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga. Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino. Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi, ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga. Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe. Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala; ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta. Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu. Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu; kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu; kuti Inu Yehova munachichita. Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera. Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda. Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:18-19

Koma zakutuluka m'kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:21

Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:28

Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:6

Mau a oipa abisalira mwazi; koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:6

Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:69

Odzikuza anandipangira bodza: Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:21

Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:9

Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:11

Mboni za chiwawa ziuka, zindifunsa zosadziwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:4

kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:10

Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:19

Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:3

Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:7

Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:12-14

Pakuti si mdani amene ananditonzayo; pakadatero ndikadachilola, amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida; pakadatero ndikadambisalira: Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane. Tinapangirana upo wokoma, tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:25

Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:33

Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:3

Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa machindwi a nyumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:31-32

M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; koma lilime lokhota lidzadulidwa. Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:5-6

Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika. Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika; koma mdani apsompsona kawirikawiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:24-26

Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake. Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri. Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:17-18

Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali. Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:37

Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:17-18

Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:3-4

Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira; amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:12-15

Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota. Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu. Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:15

Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:7

M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:28

Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:6

Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:3

Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:9

Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:8

Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:14

Anzeru akundika zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:34

Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1

Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:17-18

Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:23

Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:14-16

Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza. Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba. Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:17

Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:6

Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:28

Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:5

Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:12

Wopeputsa mnzake asowa nzeru; koma wozindikira amatonthola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:18-19

Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa, momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:10

Ndipo amene aliyense adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:4

M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu wabwino ndi wolungama, njira zanu zonse ndi zolunjika ndi zangwiro, mulibe choipa, ndinu wabwino ndi waulemu. Ndaona ulemerero wanu m'moyo wanga, kangapo mwanditsogolera kukhala chete kuti ndione chitetezo chanu, chifukwa simunandisiye m'manja mwa adani anga, koma mwatseka pakamwa pawo kuti ndisachite manyazi. Chifukwa cha ichi lero ndikukuthokozani ndi kukupatsani ulemerero wonse chifukwa dzanja lanu lamphamvu landigwira, ndimayimirira chifukwa cha chilungamo chanu, chifukwa cha chikondi chanu chosatha ndi choonadi. Tsiku lililonse ndikufuna kukhala pamaso panu m'njira yoti khalidwe la Khristu liwonekere m'moyo wanga, ndikufuna kuyenda molunjika ndikusunga mawu anu nthawi zonse, osayang'ana zomwe anthu angandichite kapena kundiuza, ndidzakhulupirira inu chifukwa mudzamasula moyo wanga kachiwiri. Chifukwa chake ndikuyembekezera inu chifukwa ndodo yanu ndi chibonga chanu zidzandilimbikitsa. Zikomo, Ambuye, pa chilichonse, pa zomwe sindimvetsetsa ndi zoyipa zomwe anandichitirapo. Lero ndikupemphani kuti mukhululukire onse omwe adanyamuka kundinenera zabodza ndipo ndikuwalengeza omasuka m'dzina la Yesu. Ndikukupemphaninso kuti musunge pakamwa panga ku chinyengo, ndi kumasula lilime langa kuti lisanene bodza, kuti zolinga zanga zikhale zoona nthawi zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa