Za ufumu wa Mfumu yokomaSalimo la Solomoni. 1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu. 2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo, ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo. 3 Mapiri adzatengera anthu mtendere, timapiri tomwe, m'chilungamo. 4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa. 5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi, kufikira mibadwomibadwo. 6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko. 7 Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. 8 Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi. 9 Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka. 10 Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso. 11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira. 12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. 13 Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. 14 Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake. 15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse. 16 M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi. 17 Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala. 18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo. 19 Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen. 20 Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi