Moyoyo wanga, dziko lino lili ndi zinthu zambiri zosadziwika. Palibe amene akudziwa bwino zomwe zidzachitike mawa, kapena patapita nthawi. Koma tili ndi chiyembekezo mwa Mulungu, amene anatikondera kwambiri moti anatipatsa Mwana wake yekhayo kuti tipulumuke.
Iye akukonzerera malo athu kumwamba, ndipo palibe chilichonse chingatilekanitse ndi chikondi chake. Monga mmene lemba la Masalmo 71:5 limanenera, “Pakuti Inu, Ambuye Yehova, ndinu chiyembekezo changa, chitetezo changa kuyambira ndili mwana.”
Ngakhale kuti dziko lino lili ndi mavuto ambiri, ife Akhristu timayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu, podalira chikondi chake chosatha. Ngakhale mphepo yamkuntho ikabvumba boti lathu, sitidzalowa m'madzi, chifukwa Yesu adzatithandiza.
Tsiku ndi tsiku, timapempha Mzimu Woyera kuti ulimbitse chikhulupiriro chathu, kuti tisagonje pamene tavutika, ndi kuti tizindikire kuti Yesu wapambana kale zonse, ndipo m'dzina lake ndife opambana. Timadziwa kuti tidzakumana ndi mavuto, koma Yesu Khristu amatipatsa mphamvu zopirira ndi kupitiriza ulendo wathu.
Ameni.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.
Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu; ndipo Yehova adzandipulumutsa. Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga. Anaombola moyo wanga kunkhondo, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.
Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha: Mundiphunzitse malemba anu.
Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza. Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,
Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;
Ndili nacho chiyembekezo popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu. Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife, kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani! Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;