Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 13:5 - Buku Lopatulika

Pomwepo anathira madzi m'beseni, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atatero adathira madzi m'beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaŵapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m'chiwuno.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.

Onani mutuwo



Yohane 13:5
30 Mawu Ofanana  

nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;


Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.


Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.


Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.


Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.


Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.


Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.


naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.


Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.


Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.


Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?


Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.


koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.


Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Pamenepo anamlonga m'nyumba yake, napatsa abulu chakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.


Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.